MlimiPay

Chidziwitso kwa alimi

Chonde werengani izi musanalipiriretu.

  1. 1

    Kulipiriratu ndi MlimiPay ndi kulipira zipangizo za ulimi zenizeni (mwachitsanzo mbewu kapena feteleza) zomwe mwasankha.

  2. 2

    Si ndalama zosungitsa ku banki, si ngongole komanso si investment. Sizipeza chiwongola dzanja.

  3. 3

    Ndalama zanu zimapatulidwa kuti zigule zipangizo. Zipangizo zanu zimasungidwa mukamaliza kulipira phukusi lonse.

  4. 4

    Mumalandira SMS pa malipiro aliwonse. Isungeni ngati umboni wanu.

  5. 5

    Ngati mukufuna kusiya kapena kusintha phukusi lanu, imbani nambala yothandizira. Tikufotokozerani momwe kubwezera ndalama kumagwirira ntchito.

  6. 6

    Ogwira ntchito a MlimiPay sadzakufunsani PIN yanu ya mobile money.

Chidziwitsochi chikuyembekezera kuwunikidwa ndi loya tisanatsegule.